Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.
2 Samueli 13:26 - Buku Lopatulika Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Abisalomu anati, Ngati nkutero, mulole mbale wanga Aminoni apite nafe. Ndipo mfumu inanena naye, Iye apitirenji nawe? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Abisalomu adati, “Chabwino, ngati inu simupita, bwanji apite nao ndi mbale wanga Aminoniyu.” Apo mfumu idafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukufuna kuti iyeyu apite nao?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.” Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?” |
Ndipo mfumu inati kwa Abisalomu, Iai mwana wanga, tisapite tonse, kuti tingakuchulukire. Ndipo iye anaiumirira koma inakana kupita; koma inamdalitsa.
Koma Abisalomu anaiumirira iyo, nilola kuti Aminoni ndi ana aamuna onse a mfumu apite naye.
Ndipo Yowabu ananena ndi Amasa, Uli bwino mbale wanga? Ndipo Yowabu anagwira ndevu za Amasa ndi dzanja lake lamanja kuti ampsompsone.
Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?