Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
2 Samueli 12:15 - Buku Lopatulika Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pompo Natani adabwerera kunyumba kwake. Motero Chauta adalanga mwana amene mkazi wa Uriya adabalira Davide, ndipo adadwala kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala. |
Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.
Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.
Ndipo Yehova anadwaza mfumu, nakhala iye wakhate mpaka tsiku la imfa yake, nakhala m'nyumba ya padera. Ndipo Yotamu mwana wa mfumu anayang'anira banja la mfumu, naweruza anthu a m'dziko.
Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa; mukalanda mpweya wao, zikufa, ndipo zibwerera kufumbi kwao.
Ndipo pomwepo mngelo wa Ambuye anamkantha, chifukwa sanampatse Mulungu ulemerero; ndipo anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.
Tapenyani tsopano kuti Ine ndine Iye, ndipo palibe mulungu koma Ine; ndipha Ine, ndikhalitsanso ndi moyo, ndikantha, ndichizanso Ine; ndipo palibe wakulanditsa m'dzanja langa.
Nati Davide, Pali Yehova, Yehova adzamkantha iye; kapena tsiku la imfa yake lidzafika; kapena adzatsikira kunkhondo, nadzafako.