Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 12:16 - Buku Lopatulika

16 Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Chifukwa chake Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu; Davide nasala kudya, nalowa, nagona usiku wonse pansi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Nchifukwa chake Davide adapempherera mwanayo kwa Mulungu. Adaleka kudya, nakaloŵa m'nyumba, nkukagona pansi usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 12:16
17 Mawu Ofanana  

Ndipo Natani anamuka kwao. Ndipo Yehova anadwaza mwana amene mkazi wa Uriya anambalira Davide, nadwala kwambiri.


Nati iye, Pamene mwanayo akali ndi moyo, ndinasala kudya ndi kulira, pakuti ndinati, Adziwa ndani kapena Yehova adzandichitira chifundo kuti mwanayo akhale ndi moyo.


Pamenepo mfumu inanyamuka ning'amba zovala zake nigona pansi, ndipo anyamata ake onse anaimirirapo ndi zovala zao zong'ambika.


Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a.


Ndipo kunali, pakumva mau awa, ndinakhala pansi ndi kulira misozi, ndi kuchita maliro masiku ena, ndinasalanso, ndi kupemphera pamaso pa Mulungu wa Kumwamba,


Muka, sonkhanitsa Ayuda onse opezeka mu Susa, nimundisalire, osadya osamwa masiku atatu, usiku ndi usana, ine ndemwe ndi anamwali anga tidzasala momwemo, ndipo motero ndidzalowa kwa mfumu, ndiko kosalingana ndi lamulo; ndikaonongeka tsono ndionongeke.


Ndipo undiitane tsiku la chisautso, ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.


Ndipo ndinalira pa kusala kwa moyo wanga, koma uku kunandikhalira chotonza.


Ndipo tsiku limenelo Ambuye, Yehova wa makamu, anaitana kulira, ndi kugwa misozi, ndi kumeta, ndi kuvala chiguduli m'chuuno;


Yehova, iwo adza kwa Inu movutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.


Pamenepo mfumu inamuka kuchinyumba chake, nichezera kusala usikuwo, ngakhale zoimbitsa sanabwere nazo pamaso pake, ndi m'maso mwake munamuumira.


Ndipo ndinaika nkhope yanga kwa Ambuye Mulungu, kumfunsa Iye m'pemphero, ndi mapembedzero, ndi kusala, ndi ziguduli, ndi mapulusa.


Kaya, akatembenuka Mulungu, ndi kuleka kubwera ku mkwiyo wake waukali, kuti tisatayike.


Ndipo anakhala masiku atatu wosaona, ndipo sanadye kapena kumwa.


Ndipo Yoswa anang'amba zovala zake, nagwa nkhope yake pansi, ku likasa la Yehova, mpaka madzulo, iye ndi akuluakulu a Israele, nathira fumbi pamitu pao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa