Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.
2 Samueli 11:14 - Buku Lopatulika Ndipo m'mawa Davide analembera Yowabu kalata, wopita naye Uriya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo m'mawa Davide analembera Yowabu kalata, wopita naye Uriya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa M'maŵa mwake Davide adalembera Yowabu kalata, napatsira Uriya yemweyo kalatayo kuti akapereke. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. |
Chifukwa ninji unapeputsa mau a Yehova ndi kuchita chimene chili choipa pamaso pake? Unakantha Uriya Muhiti ndi lupanga ndi kutenga mkazi wake akhale mkazi wako; ndipo unamupha iye ndi lupanga la ana a Amoni.
Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama; zisachite ufumu pa ine. Pamenepo ndidzakhala wangwiro, ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.
Indetu, anthu achabe ndi mpweya, ndipo anthu aakulu ndi bodza, pakuwayesa apepuka; onse pamodzi apepuka koposa mpweya.