Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.
2 Akorinto 6:3 - Buku Lopatulika osapatsa chokhumudwitsa konse m'chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 osapatsa chokhumudwitsa konse m'chinthu chilichonse, kuti utumikiwo usanenezedwe; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Sitifuna kupatsa anthu chifukwa chonyozera ntchito yathu, nchifukwa chake sitikhumudwitsa munthu aliyense ndi kanthu kalikonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. |
Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.
koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.
ndipo tiopa ife kuti ntchito yathuyi idzayamba kunyonyosoka; komanso kuti Kachisi wa mulungu wamkazi Aritemi adzayamba kuyesedwa wachabe; ndiponso kuti iye adzayamba kutsitsidwa ku ukulu wake, iye amene a mu Asiya onse, ndi onse a m'dziko lokhalamo anthu, ampembedza.
Chifukwa chake tisaweruzanenso wina mnzake; koma weruzani ichi makamaka, kuti munthu asaike chokhumudwitsa panjira ya mbale wake, kapena chomphunthwitsa.
Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.
Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.
Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.