Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 8:20 - Buku Lopatulika

20 ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Sitikufuna kupatsa anthu chifukwa choti azitinenera zoipa pa mayendetsedwe athu a zopereka zachifundo zochulukazi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 8:20
9 Mawu Ofanana  

Ndipo sanawerengere anthu, amene anapereka ndalamazi m'manja mwao kuti apatse ogwira ntchito; popeza anachita mokhulupirika.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Chifukwa chake musalole chabwino chanu achisinjirire.


Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi makalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.


Koma chimene ndichita, ndidzachitanso, kuti ndikawadulire chifukwa iwo akufuna chifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.


ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;


pakuti tikonzeratu zinthu zokoma, si pamaso pa Ambuye pokha, komanso pamaso pa anthu.


Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru;


Mupewe maonekedwe onse a choipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa