Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 8:19 - Buku Lopatulika

19 ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 ndipo si ichi chokha, komanso anasankhika ndi Mipingo, apite limodzi ndi ife m'chisomo ichi, chimene tichitumikira ife, kwa ulemerero wa Ambuye, ndi kuonetsa chivomerezo chathu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ndipo si pokhapo ai, komanso mipingo idamsankha kuti adzatiperekeze pokapereka zopereka zachifundozi. Tikukonza zimenezi kuti tichitire Ambuye ulemu, ndiponso kuti tiwonetse mtima wathu wofuna kuthandiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 8:19
20 Mawu Ofanana  

Ndipo pamene anawaikira akulu mosankha mu Mpingo uliwonse, ndi kupemphera pamodzi ndi kusala kudya, naikiza iwo kwa Ambuye amene anamkhulupirirayo.


Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m'gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:


chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,


Pamene anatuma ku Masedoniya awiri a iwo anamtumikira, Timoteo ndi Erasto, iye mwini anakhalabe nthawi mu Asiya.


Ndipo m'mzinda monse munachita piringupiringu, nathamangira onse pamodzi ku bwalo losewera, atagwira Gayo ndi Aristariko, anthu a ku Masedoniya, alendo anzake a Paulo.


Ndipo si chotero chokha, koma ife tikondwera ndi Mulungu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene talandira naye tsopano chiyanjanitso.


Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi;


Pakuti zonsezi nza kwa inu, kuti chisomocho, chochulukitsidwa mwa unyinjiwo, chichulukitsire chiyamiko ku ulemerero wa Mulungu.


Koma tsopano tsirizani kuchitaku; kuti monga kunali chivomerezo cha kufunira, koteronso kukhale kutsiriza kwake m'chimene muli nacho.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


ndi kupewa ichi kuti wina angatitchule za kuchulukira kumene tikutumikira;


pakuti ndidziwa chivomerezo chanu chimene ndidzitamandira nacho chifukwa cha inu ndi Amasedoniya, kuti Akaya anakonzekeratu chitapita chaka; ndi changu chanu chinautsa ochulukawo.


Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa