Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera makalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo;
2 Akorinto 3:1 - Buku Lopatulika Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, makalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi tilikuyambanso kudzivomereza tokha? Kapena kodi tisowa, monga ena, akalata otivomerezetsa kwa inu, kapena ochokera kwa inu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi ponena izi ndiye kuti tikuyamba kudzichitira umboni tokha? Kodi kapena nkofunika kuti ifenso, monga anthu ena, tikhale ndi makalata otichitira umboni kwa inu, kapena makalata aumboni ochokera kwa inu? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena? |
Ndipo pamene iye anafuna kuoloka kunka ku Akaya, abale anamfulumiza, ndi kulembera makalata kwa ophunzira kuti amlandire: ndipo pamene anafika, iye anathangata ndithu iwo akukhulupirira mwa chisomo;
Ndipereka kwa inu Febe, mlongo wathu, ndiye mtumiki wamkazi wa Mpingo wa Ambuye wa ku Kenkrea;
monga inenso ndikondweretsa onse m'zinthu zonse, wosafuna chipindulo changa, koma cha unyunjiwo, kuti apulumutsidwe.
Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi makalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.
Monga mwa chisomo cha Mulungu chidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.
Pakuti mungakhale muli nao aphunzitsi zikwi khumi mwa Khristu, mulibe atate ambiri; pakuti mwa Khristu Yesu ine ndinabala inu mwa Uthenga Wabwino.
Pakuti sitilimba mtima kudziwerenga, kapena kudzilinganiza tokha ndi ena a iwo amene adzivomeretsa okha; koma iwowa, podziyesera okha ndi iwo okha, ndi kudzilinganiza okha ndi iwo okha, alibe nzeru.
Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;
Ndakhala wopanda nzeru, mwandichititsa kutero; pakuti inu munayenera kundivomereza; pakuti sindiperewere ndi atumwi oposatu m'kanthu konse, ndingakhale ndili chabe.
Mumayesa tsopano lino kuti tilikuwiringula kwa inu. Tilankhula pamaso pa Mulungu mwa Khristu. Koma zonse, okondedwa, zili za kumangirira kwanu.
Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.
Sitidzivomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu chifukwa cha kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.