Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Akorinto 12:4 - Buku Lopatulika

kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kumeneko munthuyo adamva zinthu zosasimbika, zinthu zimene munthu sangazilankhule.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena.

Onani mutuwo



2 Akorinto 12:4
9 Mawu Ofanana  

Ndinaupanga wokoma ndi nthawi zake zochuluka; ndi mitengo yonse ya mu Edeni inali m'munda wa Mulungu inachita nao nsanje.


Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati padziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje.


Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine mu Paradaiso.


Ndipo pamene anakwera kutuluka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonenso, pakuti anapita njira yake wokondwera.


Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira.


Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.


pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.


Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye amene apambana ndidzampatsa kudya za ku mtengo wa moyo umene uli mu Paradaiso wa Mulungu.