Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo pamene anakwera kutuluka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonenso, pakuti anapita njira yake wokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo pamene anakwera kutuluka m'madzi, Mzimu wa Ambuye anakwatula Filipo; ndipo mdindo sanamuonanso, pakuti anapita njira yake wokondwera.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Pamene adatuluka m'madzimo, Mzimu wa Ambuye adamchotsapo Filipo uja. Ndipo nduna ija siidamuwonenso, koma idapitirira ulendo wake ikusangalala.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Pamene iwo anatuluka mʼmadzimo, Mzimu wa Ambuye anamukwatula Filipo, ndipo Ndunayo sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:39
29 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.


Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya paphiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza.


Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.


Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse.


Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo.


Pamenepo unandikweza mzimu, nudza nane kuchipata cha kum'mawa cha nyumba ya Yehova choloza kum'mawa; ndipo taonani, pa chitseko cha chipata amuna makumi awiri mphambu asanu; ndipo ndinaona pakati pao Yazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya, akalonga a anthu.


Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.


Dzanja la Yehova linandikhalira, ndipo anatuluka nane mu mzimu wa Yehova, nandiika m'kati mwa chigwa, ndicho chodzala ndi mafupa;


Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.


Ndipo anatambasula chonga dzanja, nandigwira tsitsi la pamutu panga; ndipo mzimu unandilengetsa pakati padziko ndi thambo, numuka nane m'masomphenya a Mulungu ku Yerusalemu, ku chitseko cha chipata cha bwalo la m'katimo loloza kumpoto, kumene kunali mpando wa fano la nsanje lochititsa nsanje.


Ufumu wa Kumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m'munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m'kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.


Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m'madzi, anaona Iye thambo litang'ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:


Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.


Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.


Ndipo Mzimu anati kwa Filipo, Yandikira, nudziphatike kugaleta uyu.


Ndipo anamuuza kuti aimitse galeta; ndipo anatsikira onse awiri kumadzi, Filipo ndi mdindoyo; ndipo anambatiza iye.


Ndipo panakhala chimwemwe chachikulu m'mzindamo.


amene ife tikhoza kulowa naye ndi chikhulupiriro m'chisomo ichi m'mene tilikuimamo; ndipo tikondwera m'chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu.


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse: ndibwerezanso kutero, kondwerani.


Koma tsopano mudzitamandira m'kudzikuza kwanu; kudzitamandira kulikonse kotero nkoipa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa