Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 12:2 - Buku Lopatulika

2 Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndidziwa munthu wa mwa Khristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwachitatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndikudziŵa mkhristu wina amene adaatengedwa mwadzidzidzi kupita Kumwambamwamba. Papita zaka khumi ndi zinai chichitikire cha zimenezi. Sindidziŵa ngati zidaachitika ali m'thupi kapena ali kunja kwa thupi. Akudziŵa ndi Mulungu zimenezi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 12:2
40 Mawu Ofanana  

Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.


Kodi Mulungu adzakhala ndithu padziko lapansi? Taonani, thambo ndi mu Mwambamwamba zichepa kukulandirani, koposa kotani nanga nyumba iyi ndaimangayi.


Ndipo ananena naye, Taonani, tsono anyamata anufe tili nao amuna makumi asanu amphamvu, amuke kukafuna mbuye wanu; kapena wamkweza mzimu wa Yehova ndi kumponya paphiri lina, kapena m'chigwa china. Koma anati, Musatumiza.


Mlemekezeni, m'mwambamwamba, ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.


Pakuti atero Iye amene ali wamtali wotukulidwa, amene akhala mwachikhalire, amene dzina lake ndiye Woyera, Ndikhala m'malo aatali ndi oyera, pamodzi ndi yense amene ali wa mzimu wosweka ndi wodzichepetsa, kutsitsimutsa mzimu wa odzichepetsa, ndi kutsitsimutsa mtima wa osweka.


Ndipo mzimu unandikweza, nufika nane m'masomphenya mwa mzimu wa Mulungu kudziko la Ababiloni, kwa andendewo. M'mwemo masomphenya ndidawaona anandichokera, nakwera.


Ndipo mzimu unandinyamula numuka nane kubwalo la m'kati; ndipo taonani, ulemerero wa Yehova unadzaza Kachisi.


Ndipo kunali, pakuwadalitsa Iye analekana nao, natengedwa kunka Kumwamba.


Iye wakudya thupi langa ndi kumwa mwazi wanga akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye.


iwo anamva, nathawira kumizinda ya Likaoniya, Listara ndi Deribe, ndi dziko lozungulirapo:


Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,


Moni kwa Apelesi, wovomerezedwayo mwa Khristu. Moni iwo a kwa Aristobulo.


Mupereke moni kwa Prisika ndi Akwila, antchito anzanga mwa Khristu Yesu,


Moni kwa Androniko ndi Yunia, anansi anga, ndi andende anzanga, amene ali omveka mwa atumwi, amenenso ananditsogolera ine mwa Khristu.


Moni kwa Urbano wantchito mnzathu mwa Khristu, ndi Stakisi wokondedwa wanga.


Chifukwa chake tsopano iwo akukhala mwa Khristu Yesu alibe kutsutsidwa.


Koma kwa Iye muli inu mwa Khristu Yesu, amene anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu, ndi chilungamo ndi chiyeretso ndi chiombolo;


Chifukwa ninji? Chifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.


Dziyeseni nokha, ngati muli m'chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa.


Chifukwa chake ngati munthu aliyense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Koma ndinali wosadziwika nkhope yanga kwa Mipingo ya ku Yudeya ya mwa Khristu;


Pakuti mwa Khristu Yesu kapena mdulidwe kapena kusadulidwa kulibe mphamvu; komatu chikhulupiriro, chakuchititsa mwa chikondi.


Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.


Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.


pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.


Popeza tsono tili naye Mkulu wa ansembe wamkulu, wopyoza miyamba, Yesu mwana wa Mulungu, tigwiritsitse chivomerezo chathu.


Pakuti Khristu sanalowe m'malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza oonawo; komatu mu Mwamba momwe, kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife;


Ndinagwidwa ndi Mzimu tsiku la Ambuye, ndipo ndinamva kumbuyo kwanga mau aakulu, ngati a lipenga,


Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo: ndipo anakwatulidwa mwana wake amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wake.


Pomwepo ndinakhala mwa Mzimu; ndipo, taonani padaikika mpando wachifumu mu Mwamba ndi pa mpandowo padakhala wina;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa