Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka chakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.
1 Samueli 9:1 - Buku Lopatulika Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Panali munthu wina wotchuka, wa ku dera la Benjamini, dzina lake Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, wa fuko la Benjamini. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Panali munthu wina wa fuko la Benjamini, wotchuka, dzina lake Kisi, mwana wa Abieli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. |
Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka chakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.
Panali Myuda m'chinyumba cha ku Susa, dzina lake ndiye Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi Mbenjamini;
Zoweta zakenso zinali nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri, ndi ngamira zikwi zitatu, ndi ng'ombe zamagoli mazana asanu, ndi abulu aakazi mazana asanu, antchito ake omwe ndi ambiri; chotero munthuyu anaposa anthu onse a kum'mawa.
Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai.
Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa ndipo anthu onse anamlekeza m'chifuwa.
Ndipo panali munthu ku Maoni, amene katundu wake anali ku Karimele; iyeyu anali womveka ndithu, anali nazo nkhosa zikwi zitatu, ndi mbuzi chikwi chimodzi; ndipo analikusenga nkhosa zake ku Karimele.