Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka.
1 Samueli 8:12 - Buku Lopatulika idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ena idzaŵaika kuti akhale olamulira ankhondo chikwi chimodzi kapena makumi asanu. Ndipo ena azidzalima kumunda kwake ndi kumakolola zolima zake, kusula zida zankhondo ndiponso zipangizo za magaleta ankhondo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. |
Ndipo Solomoni anali nao akapitao khumi ndi awiri akuyang'anira Aisraele onse, akufikitsira mfumu ndi banja lake zakudya; aliyense anafikitsa zakudya zofikira mwezi umodzi wa chaka.
Ndipo Mose anakwiya nao akazembe a nkhondoyi, atsogoleri a zikwi, atsogoleri a mazana, akufuma kunkhondo adaithira.
Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yampesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;