Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 8:11 - Buku Lopatulika

11 Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu aamuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Adati, “Izi ndizo zimene mfumu yanuyo izidzakuchitani: izidzakulandani ana anu aamuna kuti akhale ankhondo, ena pa magaleta ake ankhondo, ena pa akavalo ake, ndipo ena othamanga patsogolo pa magaletawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 8:11
14 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali, chitapita ichi Abisalomu anadzikonzera galeta ndi akavalo ndi anthu makumi asanu akuthamanga momtsogolera.


Pamenepo Adoniya mwana wa Hagiti anadzikuza, nati, Ndikhala mfumu ndine; nadzikonzera agaleta ndi apakavalo ndi anthu makumi asanu omtsogolera mothamanga.


Ndipo Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi apakavalo; anali nao magaleta chikwi chimodzi mphambu mazana anai, ndi apakavalo zikwi khumi mphambu ziwiri, nawasungira m'mizinda yosungamo magaleta, ndi kwa mfumu mu Yerusalemu.


Ndipo achinyamata anzake ananena naye, nati, Mzitero ndi anthu awa adalankhula nanu, nati, atate wanu analemeretsa goli lathu, koma inu mutipepuzire limenelo; mzitero nao, Kanense wanga adzaposa m'chuuno mwa atate wanga.


Atate wanu analemeretsa goli lathu, ndipo inu tsono pepuzaniko ntchito zosautsa za atate wanu, ndi goli lolemera lake limene anatisenza, ndipo tidzakutumikirani.


Ndipo mfumu Rehobowamu anapanga m'malo mwa izo zikopa zina zamkuwa, nazipereka m'manja a akapitao a olindirira, akusunga pakhomo pa nyumba ya mfumu.


Ndipo dzanja la Yehova linakhala pa Eliya; namanga iye za m'chuuno mwake, nathamanga m'tsogolo mwa Ahabu ku chipata cha Yezireele.


Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake.


Ndipo panali nkhondo yowawa ndi Afilisti masiku onse a Saulo; ndipo Saulo pakuona munthu wamphamvu, kapena ngwazi, anamtenga akhale naye.


Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake akuima chomzinga, Imvani tsopano, inu a Benjamini; kodi mwana wa Yese adzakupatsani inu nonse minda, ndi minda yampesa, kodi adzakuikani mukhale atsogoleri a zikwi ndi a mazana;


Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa