ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.
1 Samueli 8:1 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake aamuna akhale oweruza a Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake amuna akhale oweruza a Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Samuele atakalamba, adaika ana ake kuti akhale oweruza Aisraele. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Samueli atakalamba anasankha ana ake kuti akhale oweruza Aisraeli. |
ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.
Ndikuchitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Khristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosachita kanthu monga mwa tsankho.
Ndipo anali nao ana aamuna makumi atatu okwera pa ana a abulu makumi atatu, iwo ndipo anali nayo mizinda makumi atatu, otchedwa midzi ya Yairi, mpaka lero lino, ndiyo m'dziko la Giliyadi.
Ndipo anali nao ana aamuna makumi anai ndi zidzukulu zazimuna makumi atatu, akuyenda okwera pa ana a abulu makumi asanu ndi awiri; naweruza Israele zaka zisanu ndi zitatu.
Inu akuyenda okwera pa abulu oyera, inu akukhala poweruzira, ndi inu akuyenda m'njira, fotokozerani.
Ndipo tsopano, siyi mfumu idzayendabe pamaso panu; ndipo ine ndine wokalamba waimvi; ndipo, onani, ana anga aamuna ali nanu, ndipo ine ndinayendabe pamaso panu kuyambira ubwana wanga kufikira lero.