Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 8:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli atakalamba anasankha ana ake kuti akhale oweruza Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake aamuna akhale oweruza a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake amuna akhale oweruza a Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Samuele atakalamba, adaika ana ake kuti akhale oweruza Aisraele.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 8:1
9 Mawu Ofanana  

Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.


Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.


Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi.


Iye anali ndi ana aamuna makumi anayi ndi zidzukulu makumi atatu, amene ankakwera pa abulu 70. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi zitatu.


“Inu okwera pa abulu oyera, okhala pa zishalo, ndi inu oyenda pa msewu, yankhulani.


Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa