ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Saulo.
1 Samueli 7:1 - Buku Lopatulika Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu a ku Kiriyati-Yearimu adadzatenga Bokosi lachipanganolo nakafika nalo ku nyumba ya Abinadabu pa phiri. Ndipo adasankha mwana wake, Eleazara, kuti akhale woyang'anira Bokosilo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo. |
ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Saulo.
Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
Ndipo malire analembedwa nazungulira ku mbali ya kumadzulo kunka kumwera, kuchokera kuphiri pokhala patsogolo pa Betehoroni, kumwera kwake; ndi matulukiro ake anali ku Kiriyati-Baala, womwewo ndi Kiriyati-Yearimu, mzinda wa ana a Yuda; ndiyo mbali ya kumadzulo.
Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.
Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.
Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.