Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 7:1 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

1 Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Anthu a ku Kiriyati-Yearimu adadzatenga Bokosi lachipanganolo nakafika nalo ku nyumba ya Abinadabu pa phiri. Ndipo adasankha mwana wake, Eleazara, kuti akhale woyang'anira Bokosilo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 7:1
9 Mawu Ofanana  

Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.”


Zoonadi, tinamva za Bokosi la Chipangano ku Efurata, tinalipeza mʼminda ya ku Yaara:


Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko! Musakhudze kanthu kodetsedwa! Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova tulukanimo ndipo mudziyeretse.


Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo.


Tsono Aisraeli ananyamuka ulendo ndipo tsiku lachitatu anafika ku mizinda ya Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriati-Yearimu.


Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”


Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa