Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 7:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu mu Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikulu m'Kiriyati-Yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israele linalirira Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Kuyambira tsiku limene Bokosi lachipangano lija lidakhala ku Kiriyati-Yearimu, padapita nthaŵi yaitali ya zaka makumi aŵiri. Ndipo Aisraele onse adadandaulira Chauta kuti aŵathandize.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 7:2
13 Mawu Ofanana  

ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Saulo.


M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu.


Ndipo panalinso munthu amene ananenera m'dzina la Yehova, Uriya mwana wake wa Semaya wa ku Kiriyati-Yearimu; ndipo iye ananenera mzinda uwu ndi dziko lino monga mwa mau onse a Yeremiya;


Koma vomereza zoipa zako, kuti walakwira Yehova Mulungu wako, ndi kupatukira mwa alendo patsinde pa mitengo yaiwisi yonse, ndipo sunamvere mau anga, ati Yehova.


Adzadza ndi kulira, ndipo ndidzawatsogolera ndi mapembedzero, ndidzawayendetsa kumitsinje yamadzi, m'njira yoongoka m'mene sadzaphunthwa, pakuti ndili Atate wake wa Israele, ndipo Efuremu ali mwana wanga woyamba.


Odala ali achisoni; chifukwa adzasangalatsidwa.


Ndipo ana a Israele anayenda ulendo, nafika kumizinda yao tsiku lachitatu. Koma mizinda yao ndiyo Gibiyoni, ndi Kefira, ndi Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.


Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.


Ndipo anthu a ku Kiriyati-Yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wake wamwamuna Eleazara kuti asunge likasa la Yehova.


Ndipo Samuele analankhula ndi banja lonse la Israele nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, chotsani pakati pa inu milungu yachilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira Iye yekha; mukatero, Iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa