1 Samueli 6:1 - Buku Lopatulika Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Bokosi lachipangano la Chauta lidakhala m'dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. |
Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.
Ndipo amene anapanda kufa anagwidwa ndi mafundowo; ndi kulira kwa mzindawo kunakwera kumwamba.
Ndipo pakuuka a ku Asidodi mamawa taonani Dagoni adagwa pansi, nagona chafufumimba patsogolo pa likasa la Yehova. Ndipo iwo anatenga Dagoni namuimikanso m'malo mwake.
Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.