1 Samueli 30:2 - Buku Lopatulika nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, aakulu ndi aang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, akulu ndi ang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adatenga akazi kuti akhale akapolo, pamodzi ndi onse amene anali m'menemo, aang'ono ndi aakulu omwe. Sadaphepo ndi mmodzi yemwe, koma adaŵatenga amoyo napita nawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo. |
Indedi, kuzaza kwake kwa munthu kudzakulemekezani; chotsalira cha kuzazaku mudzachiletsa.
Ndipo Davide sadasunge wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiwulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ake ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.
Ndipo sikanasoweka kanthu, kakang'ono kapena kakakulu, ana aamuna kapena ana aakazi, kapena chuma kapena china chilichonse cha zija anazitenga iwowa; Davide anabwera nazo zonse.
Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumzindako, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo.