Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.
1 Samueli 3:20 - Buku Lopatulika Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhale mneneri wa Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhale mneneri wa Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adadziŵa kuti Chauta adamsankha Samuele kuti akhale mneneri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dera la Dani mpaka ku Beeriseba anazindikira kuti Yehova analozadi chala pa Samueli kuti akhale mneneri wake. |
Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.
kuchotsa ufumu kunyumba ya Saulo ndi kukhazika mpando wachifumu wa Davide pa Israele ndi pa Yuda, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba.
Ndipo Ayuda ndi Aisraele anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, masiku onse a Solomoni.
Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.
Ndipo ndinaukitsa mwa ana anu aneneri, ndi mwa anyamata anu Anaziri. Si momwemo, inu ana a Israele, ati Yehova?
Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,
Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.
Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.