Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:20 - Buku Lopatulika

20 ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 “Pambuyo pake adaŵapatsa oweruza kufikira nthaŵi ya mneneri Samuele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Izi zonse zinatenga zaka 450. “Zitatha izi, Mulungu anawapatsa oweruza mpaka nthawi ya mneneri Samueli.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:20
9 Mawu Ofanana  

monga kuyambira tsiku lija ndinalamulira oweruza kuyang'anira anthu anga Israele; ndipo ndidzakupumulitsa kwa adani ako onse. Yehova akuuzanso kuti Yehova adzakumangira banja.


Zedi silinachitike Paska lotere chiyambire masiku a oweruza anaweruza Israele, ngakhale m'masiku a mafumu a Israele, kapena mafumu a Yuda;


Pali ponse ndinayenda nao Aisraele onse ndinanena kodi mau ndi woweruza aliyense wa Israele, amene ndinamuuza adyetse anthu anga, ndi kuti, Mwalekeranji kundimangira nyumba yamikungudza?


Koma angakhale aneneri onse kuyambira Samuele ndi akumtsatira, onse amene analankhula analalikira za masiku awa.


Ndipo Yehova anautsa oweruza, amene anawapulumutsa m'dzanja la iwo akuwafunkha.


Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamgonjetsa Kusani-Risataimu.


Ndipo masiku akuweruza oweruzawo munali njala m'dziko. Ndipo munthu wa ku Betelehemu ku Yuda anamuka nakagonera m'dziko la Mowabu, iyeyu, ndi mkazi wake, ndi ana ake aamuna awiri.


Ndipo Yehova anatumiza Yerubaala, ndi Baraki, ndi Yefita, ndi Samuele, napulumutsa inu m'manja mwa adani anu pozungulira ponse, ndipo munakhala mosatekeseka.


Ndipo Aisraele onse, kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba anazindikira kuti Samuele anakhazikika akhale mneneri wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa