Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
1 Samueli 26:25 - Buku Lopatulika Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo Saulo anati kwa Davide, Udalitsike iwe, mwana wanga Davide; udzachita ndithu champhamvu, nudzapambana. Chomwecho Davide anamuka, ndipo Saulo anabwera kwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Saulo adauza Davide kuti, “Mulungu akudalitse mwana wanga Davide. Udzachita zazikulu, ndipo pa zonsezo udzapambana.” Choncho Davide adachokapo, ndipo Saulo adabwerera kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Sauli anawuza Davide kuti, “Yehova akudalitse iwe Davide mwana wanga. Udzachita zinthu zazikulu ndipo udzapambana.” Choncho Davide anayenda njira yake ndipo Sauli anabwerera kwawo. |
Ndipo anati, Dzina lako silidzatchedwanso Yakobo, koma Israele, chifukwa unayesana naye Mulungu ndithu, ndipo unapambana.
Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula; ndipo lilime lonse limene lidzakangana nawe m'chiweruzo udzalitsutsa. Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova, ndi chilungamo chao chimene chifuma kwa Ine, ati Yehova.
inde, analimbana ndi wamthenga nampambana; analira, nampembedza Iye; anampeza Iye ku Betele, ndi kumeneko Iye analankhula ndi ife;
Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Khristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiwa, kapena zoopsa kapena lupanga kodi?
Pakuti munthu akapeza mdani wake, adzamleka kodi kuti achoke bwino? Chifukwa chake Yehova akubwezere zabwino pa ichi unandichitira ine lero lomwe.
Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israele udzakhazikika m'dzanja lako.
Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka.