Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
1 Samueli 24:13 - Buku Lopatulika Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Uchimo utulukira mwa ochimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Paja anthu akale adati, ‘Munthu woipa, ntchito zake nzoipa.’ Motero ine sindikupwetekani, ai. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani. |
Ndipo Sarai anati kwa Abramu, kusauka kwanga kukhale pa iwe: ndakupatsa iwe mdzakazi wanga pamtima pako; ndipo pakuona kuti anatenga pakati anandipeputsa ine m'maso mwake: Yehova aweruze pakati pa iwe ndi ine.
Pamenepo mzimu unavala Amasai, ndiye wamkulu wa makumi atatuwo, nati iye, Ndife anu, Davide, tivomerezana nanu mwana wa Yese inu: mtendere, mtendere ukhale ndi inu, ndi mtendere ukhale ndi athandizi anu; pakuti Mulungu wanu akuthandizani. Ndipo Davide anawalandira, nawaika akulu a magulu.
Taona, aliyense wonena miyambi adzakunenera mwambi uwu, wakuti, Monga make momwemo mwana wake.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Potero sindinakuchimwirani ine, koma mundichitira choipa ndinu kundithira nkhondo; Yehova Woweruzayo, aweruze lero lino pakati pa ana a Israele ndi ana a Amoni.