Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,
1 Samueli 22:4 - Buku Lopatulika Ndipo anawatenga kunka nao pamaso pa mfumu ya Mowabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anawatenga kunka nao pamaso pa mfumu ya Mowabu; ndipo iwo anakhala naye nthawi yonse Davide anali ku lingalo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho adaŵasiya kumeneko makolo akewo kwa mfumu ya ku Mowabuko, ndipo iwo adakhala komweko nthaŵi yonse imene Davide ankabisala kuphanga kuja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho iye anawasiya kwa mfumu ya Mowabu ndipo anakhala naye nthawi yonse imene Davide ankabisala ku phanga kuja. |
Ndipo pouka Davide m'mawa mau a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlauli wa Davide, kuti,
Ndipo anakantha Amowabu nawayesa ndi chingwe, nawagonetsa pansi; ndipo anawayesera zingwe ziwiri kupha, ndi chingwe chimodzi chathunthu kusunga ndi moyo. Ndipo Amowabu anakhala anthu a Davide, nabwera nayo mitulo.
Zochita mfumu Davide tsono, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zalembedwa m'buku la mau a Samuele mlauli, ndi m'buku la mau a Natani mneneri, ndi m'buku la mau a Gadi mlauli;
Ndipo anaika Alevi m'nyumba ya Yehova ndi nsanje, ndi zisakasa, ndi azeze, monga umo adauzira Davide, ndi Gadi mlauli wa mfumu, ndi Natani mneneriyo; pakuti lamulo ili lidafuma kwa Yehova mwa aneneri ake.
Koma ndinati, Munthu ngati ine nkuthawa kodi? Ndani wonga ine adzalowa mu Kachisi kupulumutsa moyo wake? Sindidzalowamo.
Ndakhulupirira Yehova, mutani nkunena kwa moyo wanga, Thawirani kuphiri lanu ngati mbalame?
Koma pamene angakuzunzeni inu m'mudzi uwu, thawirani mwina: indetu ndinena kwa inu, Simudzaitha mizinda ya Israele, kufikira Mwana wa Munthu atadza.
Ndipo Davide anachoka kumeneko kunka Mizipa wa ku Mowabu; nati kwa mfumu ya Mowabu, Mulole atate wanga ndi mai wanga atuluke nakhale nanu, kufikira ndidziwa chimene Mulungu adzandichitira.
Ndipo mneneri Gadi anati kwa Davide, Musamakhala m'lingamo; chokani, mulowe m'dziko la Yuda. Potero Davide anachokako, nafika ku nkhalango ya Hereti.