pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.
1 Samueli 22:16 - Buku Lopatulika Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Komabe mfumu idati, “Iwe Ahimeleki, ndi onse a m'banja la bambo wako, mufa ndithu nonse!” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma mfumu inati, “Iwe Ahimeleki ndi banja lonse la abambo ako mudzaphedwa ndithu.” |
pakuti pamene Yezebele anapulula aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri zana limodzi, nawabisa makumi asanu asanu m'phanga, nawadyetsa mkate ndi madzi.
Tsono Yezebele anatuma mthenga kwa Eliya, wakuti, Milungu indilange nionjezepo, ngati sindilinganiza moyo wako ndi moyo wa mmodzi wa iwowo mawa nthawi yomwe ino.
Koma anachiyesa chopepuka kumthira manja Mordekai yekha; pakuti adamfotokozera mtundu wake wa Mordekai; potero Hamani anafuna kuononga Ayuda onse okhala mu ufumu wonse wa Ahasuwero, ndiwo a mtundu wa Mordekai.
Monga mkango wobangula ndi chilombo choyendayenda, momwemo mfumu yoipa ya anthu osauka.
Chifukwa chake mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse mu Babiloni.
Niyankha mfumu, niti kwa Ababiloni, Chandichokera chinthuchi; mukapanda kundidziwitsa lotoli ndi tanthauzo lake, mudzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zanu zidzayesedwa dzala.
Pamenepo Herode, poona kuti anampusitsa Anzeruwo, anapsa mtima ndithu, natumiza ena kukaononga tiana tonse ta mu Betelehemu ndi ta m'midzi yake yonse, takufikira zaka ziwiri ndi tating'ono tonse, monga mwa nthawi imeneyo iye anafunsitsa kwa Anzeruwo.
Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko.
Atate asaphedwere ana, ndi ana asaphedwere atate; munthu yense aphedwere tchimo lakelake.
Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.
Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.
Mfumu niuza asilikali akuima chomzinga iye, Potolokani, iphani ansembe a Yehova; chifukwa agwirizana ndi Davide, ndipo anadziwa kuti alinkuthawa, koma sanandiululire. Koma anyamata a mfumu sanafune kutambalitsa manja ao kupha ansembe a Yehova.