Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 20:31 - Buku Lopatulika

31 Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Kodi sukudziŵa kuti mwana wa Yese akakhalabe ndi moyo pa dziko lapansi, iweyo sudzakhala mfumu? Nchifukwa chake tsono, tuma anthu kuti akamtenge, abwere naye kuno, pakuti ndithudi adzafa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Mwana wa Yese akakhala ndi moyo pa dziko lapansi lino, iwe sudzakhala mfumu. Tsopano tumiza munthu akamutenge kubwera naye kwa ine, pakuti Davide ayenera kufa basi!”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 20:31
9 Mawu Ofanana  

Pamenepo mkwiyo wa Davide unayaka ndithu pa munthuyo, nati kwa Natani, Pali Yehova, munthu amene anachita ichi, ayenera kumupha;


Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?


Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu; monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.


Ndipo Saulo anamvera mau a Yonatani; nalumbira, Pali Yehova, sadzaphedwa iye.


Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?


Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?


Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.


Ichi unachichita sichili chabwino. Pali Yehova, muyenera kufa inu, chifukwa simunadikire mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Ndipo tsono, penyani mkondo wa mfumu ndi chikho cha madzi zinali kumutu kwake zili kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa