Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
1 Samueli 20:12 - Buku Lopatulika Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kumindako Yonatani adauza Davide kuti, “Chauta, Mulungu wa Aisraele, akhale mboni. Nditaŵafunsa abambo anga nthaŵi yonga yomwe ino maŵa, ngakhale mkucha, ndipo ndikapeza kuti akufuna kukuchitira chinthu chabwino, ndidzatumiza mau kuti udziŵe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe. |
Koma mfumu inaleka Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Saulo, chifukwa cha lumbiro la kwa Yehova linali pakati pa Davide ndi Yonatani mwana wa Saulo.
Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku; mwandisuntha, simupeza kanthu; mwatsimikiza mtima kuti m'kamwa mwanga simudzalakwa.
Yehova Chauta Mulungu, Yehova Chauta Mulungu, Iye adziwa, ndi Israele adzadziwa; ngati mopikisana, ngati molakwira Yehova,
Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.
Ndipo awiriwo anapangana pangano pamaso pa Yehova; ndipo Davide anakhala kunkhalango, koma Yonatani anapita kunyumba yake.