Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.
1 Samueli 2:23 - Buku Lopatulika Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono adafunsa ana akewo kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ndilikumvatu kwa anthu zonse zoipa zimene mukuchita. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ine ndikumva kuchokera kwa anthu onse za zoyipa zanuzo. |
Ndipo atate wake sadamvute masiku ake onse, ndi kuti, Watero chifukwa ninji? Ndiponso anali munthu wokongola ndithu; napondana ndi Abisalomu.
Maonekedwe a nkhope zao awachitira iwo mboni; ndipo amaonetsa uchimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! Chifukwa iwo anadzichitira zoipa iwo okha.
Ndipo mvula yakanidwa, ndipo panalibe mvula ya masika; ndipo unali ndi nkhope ya mkazi wadama, unakana manyazi.
Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.
nafuula nati, Anthuni, bwanji muchita zimenezi? Ifenso tili anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu, akulalikira kwa inu Uthenga Wabwino, wakuti musiye zinthu zachabe izi, nimutembenukire kwa Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo:
chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.
Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako.
Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.