Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
1 Samueli 2:22 - Buku Lopatulika Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsopano Eli adafika pokalamba kwambiri, ndipo ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachita Aisraele onse, ndiponso zoti anawo ankagona ndi akazi otumikira pa chipata cha chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Eli anakalamba kwambiri. Iye ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachitira Aisraeli onse, ndiponso kuti ankagona ndi akazi pa chipata cha tenti ya msonkhano. |
Ndipo panali pamene Israele anakhala m'dzikomo, Rubeni anamuka nagona ndi Biliha, mkazi wamng'ono wa atate wake: ndipo Israele anamva. Ana aamuna a Yakobo anali khumi ndi awiri:
Mibadwo ya Yakobo ndi iyi; Yosefe anali wa zaka khumi ndi zisanu ndi ziwiri analinkudyetsa zoweta pamodzi ndi abale ake; ndipo anali mnyamata pamodzi ndi ana a Biliha, ndi ana aamuna a Zilipa, akazi a atate wake; ndipo Yosefe anamfotokozera atate wake mbiri yao yoipa.
Ndipo anapanga mkhate wamkuwa, ndi tsinde lake lamkuwa, wa akalirole a akazi otumikira, akutumikira pa khomo la chihema chokomanako.
Ansembe ake achitira choipa chilamulo changa, nadetsa zopatulika zanga, sasiyanitsa pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndipo sazindikiritsa anthu pakati pa zodetsa ndi zoyera, nabisira masabata anga maso ao; ndipo Ine ndidetsedwa pakati pao.
Ndipo iye ananena nao, Mumachitiranji chotere: popeza ndilinkumva za machitidwe anu oipa kwa anthu onsewa.
Popeza ndinamuuza kuti ndidzaweruza nyumba yake kosatha chifukwa cha zoipa anazidziwa, popeza ana ake anadzitengera temberero, koma iye sanawaletse.
Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake aamuna akhale oweruza a Israele.