Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;
1 Samueli 2:20 - Buku Lopatulika Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Eli ankadalitsa Elikana ndi mkazi wake, ponena kuti, “Chauta akupatseni ana mwa mkazi ameneyu, chifukwa cha mwana amene iye adampereka kwa Chauta.” Atatero, iwowo ankabwerera kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsono Eli amadalitsa Elikana ndi mkazi wake ndi mawu akuti “Yehova akupatseni ana mwa mkazi uyu kulowa mʼmalo mwa amene anapempha ndi kumupereka kwa Yehova.” |
Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;
Ndipo sanatero kodi wina womtsalira mzimu? Ndipo winayo anatero bwanji? Anatero pofuna mbeu ya Mulungu. Koma sungani mzimu wanu; ndipo asamchitire monyenga mkazi wa ubwana wake ndi mmodzi yense.
Ndipo Simeoni anawadalitsa, nati kwa Maria amake, Taona, Uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israele; ndipo akhale chizindikiro chakutsutsana nacho;
Yehova akubwezere ntchito yako, nakupatse mphotho yokwanira Yehova, Mulungu wa Israele, amene unadza kuthawira pansi pa mapiko ake.
Pamenepo anthu onse anali kuchipata, ndi akulu, anati, Tili mboni ife. Yehova achite kuti mkazi wakulowayo m'nyumba mwako ange Rakele ndi Leya, amene anamanga nyumba ya Israele, iwo awiri; nuchite iwe moyenera mu Efurata, numveke mu Betelehemu;
nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.