Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.
1 Samueli 19:12 - Buku Lopatulika Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chomwecho Mikala anamtsitsira Davide pazenera, namuka iye, nathawa, napulumuka. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Mikala adamtulutsira Davideyo pa windo, ndipo adathaŵa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka. |
Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.
Pamenepo anawatsitsa pazenera ndi chingwe; popeza nyumba yake inali pa linga la mzinda, nakhala iye palingapo.
Ndipo ana a Saulo ndiwo Yonatani, ndi Isivi, ndi Malikisuwa; ndi maina a ana aakazi ake awiri ndi awa: dzina la woyamba ndiye Merabi, ndi dzina la mng'ono wake ndiye Mikala;