2 Samueli 17:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Ankhondo a Abisalomu atabwera kwa mkaziyo kunyumba kuja, adamufunsa kuti, “Kodi mwaonako Ahimaazi ndi Yonatani pano?” Mkazi uja adaŵayankha kuti, “Amenewo aoloka mtsinjewu.” Koma ataŵafunafuna, osaŵapeza, ankhondowo adabwerera ku Yerusalemu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?” Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu. Onani mutuwo |