za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.
1 Samueli 15:8 - Buku Lopatulika Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adamtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, ndipo adapha anthu ena onse ndi lupanga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anatenga Agagi mfumu ya Aamaleki, koma anthu ake onse anawapha ndi lupanga. |
za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.
Ndipo otsalawo anathawira ku Afeki kumzinda, ndipo linga linawagwera anthu zikwi makumi awiri mphambu asanu ndi awiri amene adatsalawo. Ndipo Benihadadi anathawa, nalowa m'mzinda, m'chipinda cha m'katimo.
Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye.
Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake, ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri, ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi, ndi ufumu wake udzamveketsa.
naulanda, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiye ndi mmodzi yense; monga anachitira Hebroni momwemo anachitira Debiri ndi mfumu yake, monganso anachitira Libina ndi mfumu yake.
Ndipo Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.
Ndipo Saulo ananena ndi Samuele, Koma ndinamvera mau a Yehova, ndipo ndinayenda njira Yehova anandituma ine, ndipo ndinabwera naye Agagi mfumu ya Amaleke, ndi Aamaleke ndinawaononga konsekonse.
Muka tsopano, nukanthe Amaleke, nuononge konsekonse zonse ali nazo, usawalekerere, koma uwaphe mwamuna ndi mkazi, mwana ndi woyamwa, ng'ombe ndi nkhosa, ngamira ndi bulu.
Ndipo anakantha Nobu ndiwo mzinda wa ansembe ndi lupanga lakuthwa, anthu aamuna ndi aakazi, ana ndi makanda, ng'ombe ndi abulu, ndi nkhosa, ndi lupanga lakuthwa.
Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;