1 Samueli 15:9 - Buku Lopatulika9 Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafune kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Koma Saulo ndi anthu anamsunga wamoyo Agagi, ndi nkhosa zokometsetsa, ndi ng'ombe, ndi zonenepa zina, ndi anaankhosa, ndi zabwino zonse sadafuna kuzitha psiti; koma zonse zoipa ndi zonyansa anaziononga konsekonse. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Koma Saulo ndi anthu amene anali nawo, sadamuphe Agagi, sadaphenso nkhosa ndi ng'ombe zabwino koposa, anaang'ombe ndi anaankhosa onenepa, ndi zonse zimene zinkaoneka zabwino. Adangoononga zimene zinali zopanda ntchito ndi zachabechabe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga. Onani mutuwo |