Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;
1 Samueli 14:12 - Buku Lopatulika Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo anthu akukabomawo adafuulira Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Tabwerani kuno, muwona!” Apo Yonatani adauza mnyamata wakeyo kuti, “Unditsate, Chauta wapereka anthuŵa m'manja mwa Aisraele.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu a ku kaboma kaja anafuwula kwa Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Bwerani kuno ndipo tikuphunzitsani phunziro.” Ndipo Yonatani anati kwa mnyamata wake. “Nditsate pakuti Yehova wapereka Afilistiwa mʼmanja mwa Aisraeli.” |
Ndipo ndinafika lero kukasupe, ndipo ndinati, Yehova Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, ngati mundiyendetsatu bwino njira yanga m'mene ndinkamo ine;
Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.
Ndipo kudzali, pakumva iwe kuwayula ku nsonga za mkandankhuku, pomwepo fulumiratu, pakuti pamenepo Yehova watuluka pamaso pako kukakantha khamu la Afilisti.
Pamenepo Amaziya anatuma mithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu mfumu ya Israele, ndi kuti, Idzani tionane maso.
Ndipo Debora anati kwa Baraki, Nyamuka; pakuti ili ndi tsikuli Yehova wapereka Sisera m'dzanja lako; sanatuluke kodi Yehova pamaso pako? Potero Baraki anatsika kuphiri la Tabori ndi amuna zikwi khumi akumtsata.
Ndipo mnzake anayankha nati, Ichi si china konse koma lupanga la Gideoni mwana wa Yowasi, munthu wa Israele; Mulungu wapereka Midiyani ndi a m'misasa onse m'dzanja lake.
Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midiyani m'dzanja lanu.
Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.
Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ichi chidzatikhalira chizindikiro.
Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake.