Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 14:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Yonatani anakwera chokwawa, ndi wonyamula zida zake anamtsata; ndi Afilisti anagwa pamaso pa Yonatani, ndi wonyamula zida zake anawapha pambuyo pake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Choncho Yonatani adakwera chokwaŵa, mnyamata wake uja akumtsata pambuyo. Tsono Yonatani adaŵathira nkhondo Afilistiwo ndi kumaŵagwetsa, mnyamata wake uja nkumaŵapha pambuyo pa iyeyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Choncho Yonatani anakwera mokwawa, ndipo mnyamata wake uja ankamutsata. Tsono Yonatani anathira nkhondo Afilisti aja namawagwetsa, ndipo mnyamata wake uja ankawapha pambuyo pa iyeyo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 14:13
10 Mawu Ofanana  

Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu; ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.


Ndipo tidzatani ndi zinthu izi? Ngati Mulungu ali ndi ife, adzatikaniza ndani?


Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


nazima mphamvu ya moto, napulumuka lupanga lakuthwa, analimbikitsidwa pokhala ofooka, anakula mphamvu kunkhondo, anapirikitsa magulu a nkhondo yachilendo.


Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.


Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.


Ndipo a ku kabomawo anayankha Yonatani ndi wonyamula zida zake, nati, Kwerani kuno kwa ife, tikuonetseni kanthu. Ndipo Yonatani, anauza wonyamula zida zake, Kwera unditsate m'mbuyo, pakuti Yehova wawapereka m'dzanja la Israele.


Kuwapha koyambako, Yonatani ndi wonyamula zida zake, anapha monga anthu makumi awiri, monga ndime ya munda yolima ng'ombe ziwiri tsiku limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa