1 Samueli 14:11 - Buku Lopatulika Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho aŵiriwo adadziwonetsa ku kaboma kankhondo ka Afilisti. Tsono Afilisti adati, “Taonani Ahebri akutuluka m'maenje m'mene ankabisala.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.” |
Pamene dzanja la Midiyani linagonjetsa Israele, ana a Israele anadzikonzera ming'ang'ala ya m'mapiri, ndi mapanga, ndi malinga chifukwa cha Midiyani.
Pamene anthu a Israele anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.
Anateronso Aisraele onse akubisala m'phiri la Efuremu, pakumva kuti Afilisti anathawa, iwo anawapirikitsa kolimba kunkhondoko.
Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.