Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 29:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo akalonga a Afilisti anati, Ahebri awa achitanji pano? Ndipo Akisi ananena kwa akalonga a Afilisti, Uyu si Davide uja mnyamata wa Saulo, mfumu ya Israele, amene wakhala nane masiku awa kapena zaka izi, ndipo sindinapeza kulakwa mwa iye, kuyambira tsiku lija anaphatikana nane kufikira lero.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Pamenepo atsogoleri aja a Afilisti adafunsa kuti, “Kodi Ahebriŵa akuchita chiyani kuno?” Akisi adayankha kuti, “Uyutu ndi Davide, mtumiki wa Saulo mfumu ya Aisraele. Iye wakhala nane tsopano masiku ambiri kapena nditi zaka, chibwerere chake kuno sindidampeze cholakwa chilichonse mpaka lero lino.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Tsono atsogoleri a Afilisti aja anafunsa kuti, “Kodi Ahebri awa akufuna chiyani?” Akisi anayankha kuti, “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Sauli mfumu ya Israeli. Iye wakhala ndi ine kwa masiku ndithu, kapena titi zaka ndipo kuyambira tsiku limene anachoka kwa Sauli mpaka lero, ine sindinapeze cholakwa mwa iye.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 29:3
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anadza wina amene anapulumuka namuuza Abramu Muhebri; ndipo iye analinkukhala pa mitengo yathundu ya pa Mamure Mwamori, mkulu wake wa Esikolo, ndi mkulu wake wa Anere; amenewo ndiwo opangana naye Abramu.


Ena a Manase omwe anapatukira kwa Davide, muja iye anadza ndi Afilisti koponyana nkhondo ndi Saulo, koma sanawathandize; popeza akalonga a Afilisti, atachita upo, anamuuza achoke, ndi kuti, Adzapatukira kwa mbuye wake Saulo ndi kutisandulikira.


Pomuka iye ku Zikilagi anapatukira kwa iye a Manase: Adina, ndi Yozabadi, ndi Yediyaele, ndi Mikaele, ndi Yozabadi, ndi Elihu, ndi Ziletai, akulu a zikwi a ku Manase.


Pamenepo anthu awa anati, Sitidzamtola chifukwa chilichonse Daniele amene, tikapanda kumtola ichi pa chilamulo cha Mulungu wake.


Ndipo pamene ansembe aakulu ndi anyamata anamuona Iye, anafuula nanena, Mpachikeni, mpachikeni. Pilato ananenana nao, Mtengeni Iye inu nimumpachike; pakuti ine sindipeza chifukwa mwa Iye.


Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.


ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.


Ndipo onse awiri anadziwulula kwa a ku kaboma ka Afilistiwo; ndipo Afilistiwo anati, Onani, Ahebri alikutuluka m'mauna m'mene anabisala.


Mukhululukire kulakwa kwa mdzakazi wanu; pakuti Yehova adzapatsadi mbuye wanga banja lokhazikika, pakuti mbuyanga amaponya nkhondo za Yehova; ndipo mwa inu simudzapezeka choipa masiku anu onse.


Ndipo Davide ananena mumtima mwake, Tsiku lina Saulo adzandipha; palibe china chondikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Saulo adzakhala kakasi chifukwa cha ine, osandifunanso m'malire onse a Israele, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lake.


Ndipo kuwerenga kwake kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko chaka chimodzi ndi miyezi inai.


Ndipo Akisi anaitana Davide, nanena naye, Pali Yehova, wakhala woongoka mtima, ndipo kutuluka kwako ndi kubwera kwako pamodzi ndi ine m'gulumo kundikomera; pakuti sindinaona choipa mwa iwe kuyambira tsiku la kufika kwako kufikira lero; koma akalongawo sakukomera mtima.


Ndipo Afilistiwo pakumva kubuma pa kufuula kwao, anati, Phokoso ili la kufuula kwakukulu ku zithando za Aisraele n'lachani? Ndipo anamva kuti likasa la Yehova lidafika ku zithandozo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa