1 Samueli 29:4 - Buku Lopatulika4 Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Koma iwo adamkalipira Akisiyo namuuza kuti, “Mumbweze munthuyo kuti abwerere ku malo amene mudampatsa. Sadzapita nafe ku nkhondo, kuwopa kuti kunkhondoko angakasanduke mdani wathu. Nanga munthu ameneyu angathe kudziyanjanitsa bwanji ndi mbuyake? Iyeyu angathe kuchita zimenezi pakupha anthu athu ali panoŵa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa? Onani mutuwo |