Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 13:9 - Buku Lopatulika

Pamenepo Saulo anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pamenepo Saulo anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho Saulo adati, “Bwera nayoni kuno nsembe yopserezayo pamodzi ndi nsembe zachiyanjano zija.” Ndipo Saulo adapereka nsembe yopsereza ija.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kotero iye anati, “Bwera nayoni nsembe yopsereza ndi nsembe ya chiyanjano.” Ndipo Sauli anapereka nsembe yopsereza.

Onani mutuwo



1 Samueli 13:9
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anamangirapo Yehova guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika. Momwemo Yehova anapembedzeka chifukwa cha dziko, ndi mliri wa pa Israele unalekeka.


Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi paguwalo la nsembe.


Khala chete mwa Yehova, numlindirire Iye; usavutike mtima chifukwa cha iye wolemerera m'njira yake, chifukwa cha munthu wakuchita chiwembu.


Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.


Usanene, Ndidzabwezera zoipa; yembekeza Yehova, adzakupulumutsa.


Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.


Kuchita chilungamo ndi chiweruzo kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.


Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;


Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;


ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;


Ndipo Saulo ananena ndi Ahiya, Bwera nalo likasa la Mulungu kuno. Pakuti likasa la Mulungu linali kumeneko masiku aja ndi ana a Israele.