Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 3:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi paguwalo la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo mfumu inapita ku Gibiyoni kukaphera nsembe kumeneko; popeza msanje waukulu unali kumeneko, Solomoni anapereka nsembe zopsereza chikwi chimodzi pa guwalo la nsembe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Nthaŵi ina mfumu idapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe, popeza kuti kumeneko ndiko kunali kachisi woposa ena. Solomoni ankapereka nsembe zopsereza pa guwa limenelo zokwanira 1,000.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 3:4
18 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.


Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.


Yehova anaonekera kwa Solomoni nthawi yachiwiri, monga momwe adamuonekera ku Gibiyoni.


ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku chihema cha Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;


Pakuti chihema cha Yehova amene Mose anapanga m'chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi.


Ndipo Solomoni analankhula ndi Aisraele onse, ndi akulu a zikwi ndi a mazana, ndi kwa oweruza, ndi kwa kalonga aliyense wa Israele, akulu a nyumba za makolo.


Ndipo Solomoni ndi khamu lonse pamodzi naye anamuka ku msanje wa ku Gibiyoni; pakuti kumeneko kunali chihema chokomanako cha Mulungu adachimanga Mose mtumiki wa Yehova m'chipululu.


Pakuti Hezekiya mfumu ya Yuda anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi zisanu ndi ziwiri; ndi akulu anapatsa msonkhano ng'ombe chikwi chimodzi, ndi nkhosa zikwi khumi; ndipo ansembe ambiri adadzipatula.


Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ya ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi makumi awiri. Momwemo mfumu ndi anthu onse anapereka nyumba ya Mulungu.


Ndipo Lebanoni sakwanira kutentha, ngakhale nyama zake sizikwanira nsembe yopsereza.


Ndipo panali chaka chomwecho, poyamba Zedekiya kukhala mfumu ya Yuda, chaka chachinai, mwezi wachisanu, kuti Hananiya mwana wa Azuri mneneri, amene anali wa ku Gibiyoni, ananena ndi ine m'nyumba ya Yehova, pamaso pa ansembe ndi pa anthu onse, kuti,


anaopa kwambiri, popeza Gibiyoni ndi mzinda waukulu, monga wina wa mizinda yachifumu, popezanso unaposa Ai kukula kwake, ndi amuna ake onse ndiwo amphamvu.


Koma mizinda ya fuko la ana a Benjamini monga mwa mabanja ao ndiyo Yeriko, ndi Betehogila, ndi Emekezizi;


Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,


Pamenepo Saulo anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa