1 Samueli 13:17 - Buku Lopatulika Ndipo owawanya anatuluka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofura, ku dera la Suwala; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo owawanya anatuluka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofura, ku dera la Suwala; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ankhondo a Filisti adatuluka kuchoka ku zithando zao m'magulu atatu. Gulu limodzi lidalunjika ku Ofura ku dziko la Suwala. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ankhondo a Afilisti anatuluka mʼmisasa yawo mʼmagulu atatu. Gulu lina linapita ku Ofiri ku dziko la Suwala. |
Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri.
Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.