1 Samueli 11:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo mu ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo m'mawa mwake Saulo anagawa anthu magulu atatu; ndipo iwowa anafika pakati pa zithandozo m'ulonda wa mamawa, nakantha Aamoni kufikira kutentha kwa dzuwa. Ndipo otsalawo anabalalika, osatsala pamodzi ngakhale awiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 M'maŵa mwake, Saulo adagaŵa anthu ake m'magulu atatu. Ndipo adaloŵa pakati pa zithando zankhondo za Aamoni m'mamaŵa kusanache, napha Aamoniwo mpaka masana dzuŵa litatentha. Tsono amene adapulumuka adangoti balala, aliyense kwayekhakwayekha. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Tsono mmawa mwake Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Mmamawa kusanache iwo analowa mʼmisasa ya Aamoni ndi kuwapha mpaka masana. Amene anapulumuka anabalalika, aliyense kwakekwake. Onani mutuwo |