Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.
1 Samueli 13:10 - Buku Lopatulika Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samuele anafika. Ndipo Saulo anamchingamira kukamlonjera iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atangomaliza kupereka nsembe yopserezayo, adangoona Samuele watulukira. Tsono Saulo adapita kukakumana naye ndi kumulonjera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atangomaliza kupereka nsembe, anangoona Samueli watulukira ndipo Sauli anapita kukamulonjera. |
Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.
Ndipo taona, Bowazi anafuma ku Betelehemu, nati kwa ocheka, Yehova akhale nanu. Namyankha iwo, Yehova akudalitseni.
Ndipo Samuele anadza kwa Saulo; ndipo Saulo anati kwa iye, Yehova akudalitseni; ine ndinachita lamulo la Yehova.
Koma mnyamata wina anauza Abigaile, mkazi wa Nabala, kuti, Onani, Davide anatumiza mithenga akuchokera kuchipululu kulonjera mbuye wathu; koma iye anawakalipira.