Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
1 Samueli 11:6 - Buku Lopatulika Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Saulo mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo mzimu wa Mulungu unamgwera Saulo mwamphamvu, pamene anamva mau awa, ndi mkwiyo wake unayaka kwambiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo atamva zimenezi, pomwepo mzimu wa Mulungu udamloŵa mwamphamvu, ndipo adapsa mtima kwabasi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli atamva mawu awo, Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwa mphamvu ndipo anakwiya kwambiri. |
Ndipo kunali, pamene anayandikiza chigono, anaona mwanawang'ombeyo ndi kuvinako; ndipo Mose anapsa mtima, nataya magome ali m'manja mwake, nawaswa m'tsinde mwa phiri.
Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.
Pamenepo mzimu wa Yehova unamdzera Yefita, napitira iye ku Giliyadi, ndi Manase, napitira ku Mizipa wa Giliyadi, ndi kuchokera ku Mizipa wa Giliyadi anapitira kwa ana a Amoni.
Ndipo mzimu wa Yehova unayamba kumfulumiza mtima ku misasa ya Dani pakati pa Zora ndi Esitaoli.
Ndipo unamgwera iye kolimba mzimu wa Yehova, naung'amba monga akadang'amba mwanawambuzi, wopanda kanthu m'dzanja lake; koma sanauze atate wake kapena amai wake chimene adachichita.
Pamene anafika ku Lehi Afilisti anafuula pokomana naye; koma mzimu wa Yehova unamgwera kolimba, ndi zingwe zokhala pa manja ake zinanga thonje lopserera ndi moto, ndi zomangira zake zinanyotsoka pa manja ake.
Ndipo unamdzera mzimu wa Yehova, iye naweruza Israele, natuluka kunkhondo; napereka Yehova Kusani-Risataimu mfumu ya Mesopotamiya m'dzanja lake; ndi dzanja lake linamgonjetsa Kusani-Risataimu.
Koma mzimu wa Yehova unavala Gideoni; naomba lipenga iye, ndi a banja la Abiyezere analalikidwa kumtsata iye.
Ndipo pamene anafika ku Gibea, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao.
ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.
Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.
Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye.