1 Samueli 1:28 - Buku Lopatulika chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 chifukwa chake inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wake aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake ndampereka kwa Chauta. Moyo wake wonse mwanayu adzakhala wake wa Chauta.” Ndipo onsewo adapembedza Chauta kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndiye tsopano ine ndikumupereka kwa Yehova. Pa moyo wake wonse adzakhala wa Yehova.” Ndipo onse anapembedza Yehova kumeneko. |
Ndipo ndinawerama mutu wanga ndi kulambira Yehova, ndi kumyamikira Yehova, Mulungu wa mbuyanga Abrahamu, amene ananditsogolera ine m'njira yakuona, kuti ndikamtengere mwana wamwamuna wake mwana wa mkazi wa mphwake wa mbuyanga.
ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu.
Ndipo kunali, pakumva Gideoni kufotokozera kwa lotolo ndi tanthauzo lake, anadziwerama; nabwera ku misasa ya Israele nati, Taukani, pakuti Yehova wapereka a m'misasa a Midiyani m'dzanja lanu.
nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.
Koma Hana sadakwere, chifukwa kuti anati kwa mwamuna wake Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako chikhalire.
Ndipo Eli anadalitsa Elikana ndi mkazi wake, nati, Yehova akupatse mbeu ndi mkazi uyu m'malo mwa iye amene munampempha kwa Yehova. Ndipo iwowa anabwera kwao.
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Potero mudzadziwe chimene mnyamata wanu adzachita. Ndipo Akisi anati kwa Davide, Chifukwa chake ndidzakuika iwe ukhale wondisungira moyo wanga masiku onse.