1 Samueli 1:2 - Buku Lopatulika Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lake ndi Hana, mnzake dzina lake ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Elikanayo anali wamitala, mkazi wina dzina lake anali Hana, winayo anali Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anali ndi akazi awiri, Hana ndi Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe. |
Ndipo Isaki anampembedzera mkazi wake kwa Yehova popeza anali wouma: ndipo Yehova analola kupembedza kwake, ndipo Rebeka mkazi wake anatenga pakati.
Pamene Yehova anaona kuti anamuda Leya, anatsegula m'mimba mwake; koma Rakele anali wouma.
Ndipo Lameki anadzitengera yekha akazi awiri: dzina lake la wina ndi Ada, dzina lake la mnzake ndi Zila.
Lameki ndipo anati kwa akazi ake, Tamvani mau anga, Ada ndi Zila; inu akazi a Lameki, mverani kunena kwanga: Ndapha munthu wakundilasa ine, ndapha mnyamata wakundipweteka ine.
Iye ananena kwa iwo, Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuchotsa akazi anu; koma pachiyambi sikunakhala chomwecho.
Ndipo panali Anna, mneneri wamkazi, mwana wa Fanuwele, wa fuko la Asere; amene anali wokalamba ndithu, nakhala ndi mwamuna wake, kuyambira pa unamwali wake,
Ndipo panali munthu wina wa Zora wa banja la Adani, dzina lake ndiye Manowa; ndi mkazi wake analibe mwana, sanabale.
Nakhala nao ana aamuna makumi asanu ndi awiri Gideoni, anawabala ndi iye; popeza anali nao akazi ambiri.