Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Akorinto 7:2 - Buku Lopatulika

Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma chifukwa cha madama munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

koma kuwopa dama, mwamuna aliyense akhale ndi mkazi wakewake, ndipo mkazi aliyense akhale ndi mwamuna wakewake.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma chifukwa choti chigololo chawanda, mwamuna aliyense akhale naye mkazi wakewake ndipo mkazi aliyense akhale naye mwamuna wakewake.

Onani mutuwo



1 Akorinto 7:2
14 Mawu Ofanana  

Wopeza mkazi apeza chinthu chabwino; Yehova amkomera mtima.


Nyumba ndi chuma ndizo cholowa cha atate; koma mkazi wanzeru achokera kwa Yehova.


Koma mukuti, Chifukwa ninji? Chifukwa kuti Yehova anali mboni pakati pa iwe ndi mkazi wa ubwana wako, amene unamchitira chosakhulupirika, chinkana iye ndiye mnzako, mkazi wa pangano lako.


koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuchotsa mkazi wake, kosati chifukwa cha chigololo, amchititsa chigololo: ndipo amene adzakwata wochotsedwayo achita chigololo.


Thawani dama. Tchimo lililonse munthu akalichita lili kunja kwa thupi; koma wachiwerewere achimwira thupi lake la iye yekha.


Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.


Mwamunayo apereke kwa mkazi mangawa ake; koma modzimodzinso mkazi kwa mwamuna.


Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.


Koteronso amuna azikonda akazi ao a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha. Wokonda mkazi wa iye yekha, adzikonda yekha;


Komanso inu, yense pa yekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga adzikonda yekha; ndipo mkaziyo akumbukire kuti aziopa mwamuna.


yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu,


a kuletsa ukwati, osiyitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti achikhulupiriro ndi ozindikira choonadi azilandire ndi chiyamiko.


Ndipo kudzali, akatifikira atate ao kapena alongo ao kunena nafe mlandu, tidzanena nao, Mutipatse awa, pakuti sitinawatengera yense mkazi wake kunkhondo; pakuti inunso simunawaninkhe awa; mukadatero mukadapalamula tsopano.